Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

EKSODO 17

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku chipululu cha Sini, ndi kumayenda malo ndi malo monga momwe anawalamulira Yehova. Iwo anamanga misasa yawo ku Refidimu koma kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa.
2Kotero iwo anakangana ndi Mose nati, “Tipatse madzi akumwa.” Mose anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukumuyesa Yehova?”
3Koma anthu anali ndi ludzu pamenepo ndipo anangʼungʼudza pamaso pa Mose namufunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto kuti ife, ana athu pamodzi ndi ziweto zathu tife ndi ludzu?”
4Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, “Kodi ndichite chiyani ndi anthu awa? Iwo atsala pangʼono kundigenda ndi miyala.”
5Yehova anati kwa Mose, “Pita patsogolo pa anthuwo. Tenga ndodo imene unamenyera nyanja ya Nailo pamodzi ndi akuluakulu ena a Israeli ndi kunyamuka.
6Ine ndidzayima patsogolo pako pafupi ndi thanthwe la ku Horebu. Ukamenye thanthwelo, madzi adzatuluka kuti anthu amwe.” Motero Mose anachita zimenezi pamaso pa akuluakulu a Israeli.
7Ndipo iye anatcha malowo Masa ndi Meriba chifukwa Aisraeli anakangana ndi kuyesa Yehova ponena kuti, “Kodi pakati pathu pali Yehova kapena palibe?”
8Amaleki anabwera ku Refidimu kudzamenyana ndi Aisraeli.
9Mose anati kwa Yoswa, “Sankha amuna amphamvu ndipo upite ukamenyane ndi Amaleki. Mawa ndidzayima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu.”
10Ndipo Yoswa anachitadi monga Mose anamulamulira. Iye anapita kukamenyana ndi Aamaleki ndipo Mose, Aaroni ndi Huri anapita pamwamba pa phiri.
11Mose ankati akakweza manja ake, Aisraeli amapambana, koma akatsitsa manja akewo Amaleki amapambana.
12Manja a Mose atatopa, Aaroni ndi Huri anatenga mwala ndi kuyika pansi ndipo Mose anakhalapo. Aaroni ndi Huri anagwirizitsa manja a Mose wina mbali ina winanso mbali ina. Choncho manja a Mose analimba mpaka kulowa kwa dzuwa.
13Kotero Yoswa anagonjetsa asilikali ankhondo a Amaleki ndi lupanga.
14Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba izi mʼbuku kuti zidzakumbukirike ndipo uwonetsetse kuti Yoswa amve zimenezi, chifukwa Ine ndidzafafaniziratu Amaleki pa dziko lapansi, kotero kuti palibe amene adzawakumbukire.”
15Mose anamanga guwa lansembe ndipo analitcha Yehova Chipambano Changa (Yehova Nisi).
16Ndipo anati, “Kwezani mbendera ya Yehova. Yehova adzachitabe nkhondo ndi mibado yonse ya Aamaleki.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.