Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

EKSODO 11

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Tsopano Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzalanga Farao pamodzi ndi Aigupto onse ndi mliri umodzi wotsiriza. Zikadzachitika izi iye adzakulolani kuti mutuluke mʼdziko lino. Ndithu pamene azidzakutulutsani adzachita ngati akukuyingitsani.
2Awuze anthu kuti mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense apemphe kwa mnansi wake ziwiya zasiliva ndi golide.”
3Tsono Yehova anachititsa Aigupto kuti akomere mtima Aisraeli. Komanso Mose anali wotchuka kwambiri mʼdziko la Igupto, pamaso pa nduna za Farao ndi anthu onse.
4Tsono Mose anawuza Farao kuti, “Pakati pa usiku, Yehova adzayenda pakati pa anthu a ku Igupto.
5Ndipo mwana aliyense wamwamuna wachisamba adzafa, kuyambira mwana wamwamuna wa Farao amene amakhala pa mpando waufumu, mpaka mwana wamwamuna wachisamba wa mdzakazi wake amene ali naye pa mtondo, komanso ana oyamba a ziweto.
6Kudzakhala kulira kwakukulu mʼdziko lonse la Igupto, kumene sikunachitikepo ndipo sikudzachitikanso.
7Koma pakati pa Aisraeli, ngakhale galu sadzawuwa munthu aliyense kapena chiweto!” Kotero mudzadziwa kuti Yehova ndiye wasiyanitsa pakati pa Igupto ndi Israeli.
8Nduna zanu zonse zidzabwera kwa ine, kugwada pamaso panga ndi kunena kuti, “Pita iwe ndi anthu ako onse amene akukutsatirawa! Zimenezi zikadzachitika ine ndidzachoka.” Ndipo Mose anachoka kwa Farao atakwiya kwambiri.
9Yehova ananena kwa Mose kuti, “Farao adzakana kukumvera, kuti zodabwitsa zanga zichuluke mʼdziko la Igupto.”
10Mose ndi Aaroni anachita zodabwitsa zonsezi pamaso pa Farao koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli atuluke mʼdziko lake.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.