Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MLALIKI 4

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Ndinayangʼananso ndi kuona chipsinjo chimene chimachitika pansi pano: ndinaona misozi ya anthu opsinjika, ndipo iwo alibe owatonthoza; mphamvu zinali ndi anthu owapsinjawo ndipo iwonso analibe owatonthoza.
2Ndipo ndinanena kuti akufa, amene anafa kale, ndi osangalala kuposa amoyo, amene akanalibe ndi moyo.
3Koma wopambana onsewa ndi amene sanabadwe, amene sanaone zoyipa zimene chimachitika pansi pano.
4Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
5Chitsiru chimangoti manja ake lobodo ndi kudzipha chokha ndi njala.
6Nʼkwabwino kukhala ndi dzanja limodzi lodzaza uli pa mtendere, kuposa kukhala ndi manja awiri odzaza uli pa mavuto, ndipo uku nʼkungodzivuta chabe.
7Ndinaonanso chinthu china chopanda phindu pansi pano:
8Panali munthu amene anali yekhayekha; analibe mwana kapena mʼbale. Ntchito yake yolemetsa sinkatha, ndipo maso ake sankakhutitsidwa ndi chuma chake. Iye anadzifunsa kuti, “Kodi ntchito yosautsayi ndikuyigwirira yani? Nanga nʼchifukwa chiyani ndikudzimana chisangalalo?” Izinso ndi zopandapake, zosasangalatsa!
9Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu:
10Ngati winayo agwa, mnzakeyo adzamudzutsa. Koma tsoka kwa munthu amene agwa ndipo alibe wina woti amudzutse!
11Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana. Koma nanga mmodzi angadzifunditse yekha?
12Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa, koma anthu awiri akhoza kudziteteza. Chingwe cha maulusi atatu sichidukirapo.
13Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo.
14Wachinyamatayo angathe kuchokera ku ndende ndi kudzakhala mfumu, kapena angathe kubadwa wosauka mʼdziko la mfumuyo.
15Ndipo ndinaona kuti iwo onse amene anakhala ndi moyo ndi kuyenda pansi pano anatsatira wachinyamatayo, amene anatenga malo a mfumu.
16Mfumu ikhoza kulamulira anthu osawerengeka, komabe itamwalira, palibe amene adzayamikire zomwe mfumuyo inachita. Izinso ndi zopandapake, nʼkungozivuta chabe.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.