Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MLALIKI 12

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Uzikumbukira mlengi wako masiku a unyamata wako, masiku oyipa asanafike, nthawi isanafike pamene udzanena kuti, “Izi sizikundikondweretsa.”
2Nthawi ya ukalamba wako, dzuwa ndi kuwala, mwezi ndi nyenyezi zidzada. Mitambo idzabweranso mvula itagwa.
3Nthawi imene manja ako adzanjenjemera, miyendo yako idzafowoka, pamene mano ako adzalephera kutafuna chifukwa ndi owerengeka, ndipo maso ako adzayamba kuchita chidima.
4Makutu ako adzatsekeka, ndipo sudzamva phokoso lakunja; sudzamvanso kusinja kwa pa mtondo kapena kulira kwa mbalame mmawa.
5Imeneyi ndiyo nthawi imene anthu amaopa kupita kumalo okwera, amaopa kuyenda mʼmisewu; Mutu umatuwa kuti mbuu, amayenda modzikoka ngati ziwala ndipo chilakolako chimatheratu. Nthawi imeneyo munthu amapita ku nyumba yake yamuyaya ndipo anthu olira maliro amayendayenda mʼmisewu.
6Kumbukira Iye chingwe cha siliva chisanaduke, kapena mbale yagolide isanasweke; mtsuko usanasweke ku kasupe, kapena mkombero usanathyoke ku chitsime.
7Iyi ndi nthawi imene thupi lidzabwerera ku dothi, kumene linachokera, mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene anawupereka.
8“Zopanda phindu! Zopandapake!” akutero Mlaliki. “Zonse ndi zopandapake!”
9Mlaliki sanali wozindikira zinthu kokha ayi, komanso ankaphunzitsa anthu. Iye ankasinkhasinkha ndi kufufuzafufuza ndi kulemba mwadongosolo miyambi yambiri.
10Mlaliki anafufuzafufuza kuti apeze mawu oyenera, ndipo zimene analemba zinali zolondola ndiponso zoona.
11Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga, zokamba zawo zimene anasonkhanitsa zili ngati misomali yokhomera, yoperekedwa ndi mʼbusa mmodzi.
12Samalira mwana wanga, za kuwonjezera chilichonse pa zimenezi. Kulemba mabuku ambiri sikutha, ndipo kuphunzira kwambiri kumatopetsa thupi.
13Basi zonse zamveka; mathero a nkhaniyi ndi awa: uziopa Mulungu ndi kusunga malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wa anthu onse.
14Pakuti Mulungu adzaweruza zochita zonse, kuphatikizanso zinthu zonse zobisika, kaya zabwino kapena zoyipa.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.