Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

MLALIKI 10

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Monga ntchentche zakufa zimayika fungo loyipa mʼmafuta onunkhira, choncho kupusa pangʼono kumawononganso nzeru ndi ulemu.
2Mtima wa munthu wanzeru umamutsogolera bwino, koma mtima wa munthu wopusa umamusocheretsa.
3Chitsiru ngakhale chikamayenda mu msewu, zochita zake ndi zopanda nzeru ndipo chimaonetsa aliyense kuti icho ndi chitsirudi.
4Ngati wolamulira akukwiyira, usachoke pa ntchito yako; kufatsa kumakonza zolakwa zazikulu.
5Pali choyipa chimene ndinachiona pansi pano, kulakwitsa kumene kumachokera kwa wolamulira:
6Zitsiru amazipatsa ntchito zambiri zapamwamba, pamene anthu olemera amawapatsa ntchito zotsika.
7Ndaona akapolo atakwera pa akavalo, pamene akalonga akuyenda pansi ngati akapolo.
8Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha; amene amabowola khoma adzalumidwa ndi njoka.
9Amene amaphwanya miyala adzapwetekedwa ndi miyalayo; amene amawaza nkhuni adzapwetekedwa nazo.
10Ngati nkhwangwa ili yobuntha yosanoledwa, pamafunika mphamvu zambiri potema, koma luso limabweretsa chipambano.
11Nʼkopanda phindu kudziwa kuseweretsa njoka ngati njokayo yakuluma kale.
12Mawu a pakamwa pa munthu wanzeru ndi okondweretsa, koma chitsiru chidzawonongedwa ndi milomo yake yomwe.
13Chitsiru chimayamba ndi mawu opusa; potsiriza pake zoyankhula zake ndi zamisala
14ndipo chitsiru chimachulukitsa mawu. Palibe amene amadziwa zimene zikubwera mʼtsogolo, ndani angamuwuze zomwe zidzachitika iye akadzafa?
15Chitsiru chimatopa msanga ndi ntchito yochepa; ndipo sichikhala ndi mphamvu zobwererera ku mudzi.
16Tsoka kwa iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ikali mwana, ndipo atsogoleri ako amakhala pa madyerero mmamawa.
17Wodala iwe, iwe dziko ngati mfumu yako ndi mwana wolemekezeka ndipo atsogoleri ako amadya pa nthawi yake, kuti apeze mphamvu osati kuti aledzere.
18Ngati munthu ndi waulesi, denga lake limaloshoka; ngati manja ake ndi alobodo nyumba yake imadontha.
19Phwando ndi lokondweretsa anthu, ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo, koma ndalama ndi yankho la chilichonse.
20Usanyoze mfumu ngakhale mu mtima mwako, kapena kutukwana munthu wachuma mʼchipinda chako, pakuti mbalame yamlengalenga itha kutenga mawu ako nʼkukafotokoza zomwe wanena.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.