Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

AMOSI 8

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: dengu la zipatso zakupsa.
2Iye anandifunsa kuti, “Amosi nʼchiyani ukuona?” Ine ndinayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.” Ndipo Yehova anati kwa ine, “Nthawi yachimaliziro yawakwanira anthu anga Aisraeli; sindidzawakhululukiranso.
3“Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akulengeza kuti, “Nyimbo za mʼNyumba ya Mulungu zidzasanduka kulira kofuwula. Mitembo ya anthu idzachuluka, ndipo adzayiponya ponseponse! Kudzangoti zii!”
4Imvani izi, inu amene mumapondereza anthu osowa ndipo simulabadira anthu osauka a mʼdzikomu.
5Mumanena kuti, “Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti kuti tigulitse zinthu? Ndipo tsiku la Sabata litha liti kuti tigulitse tirigu, kuti tichepetse miyeso, kukweza mitengo kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo,
6tigule osauka ndi ndalama zasiliva ndi osowa powapatsa nsapato, tigulitse ngakhale mungu wa tirigu?”
7Yehova amene Yakobo amamunyadira, walumbira kuti: Ine sindidzayiwala chilichonse chimene anachita.
8“Kodi dziko silidzagwedezeka chifukwa cha zimenezi, ndi onse okhala mʼmenemo kulira mwachisoni? Dziko lonse lidzavunduka ngati mtsinje wa Nailo; lidzagwedezeka kenaka nʼkukhala bata ngati mtsinje wa ku Igupto.
9“Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akunena kuti, “Ndidzadetsa dzuwa masana ndi kugwetsa mdima pa dziko lapansi dzuwa likuswa mtengo.
10Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu ndi kumeta mipala mitu yanu. Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo, ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake.
11“Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti, “Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse; osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi, koma njala yofuna kumva mawu a Yehova.
12Anthu azidzangoyendayenda kuchoka ku nyanja ina kupita ku nyanja ina. Azidzangoyendayenda kuchoka kumpoto kupita kummawa, kufunafuna mawu a Yehova, koma sadzawapeza.
13“Tsiku limenelo “anamwali okongola ndi anyamata amphamvu adzakomoka ndi ludzu.
14Onse amene amalumbira pa tchimo la Samariya, kapena kumanena kuti, ‘Iwe Dani, pali mulungu wako wamoyo,’ kapena, ‘Pali mulungu wamoyo wa ku Beeriseba.’ Iwowo adzagwa ndipo sadzadzukanso.”
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.