Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

2 AKORINTO 9

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Nʼkosafunika kuti ndikulembereni za utumiki othandiza anthu a Mulungu.
2Popeza ndikudziwa mtima wanu wofuna kuthandiza, ndipo ndakhala ndikuwawuza monyadira a ku Makedoniya za chimenechi. Ndimawawuza kuti inu a ku Akaya munakonzeka kale chaka chatha kuti mupereke. Ndipo changu chanu chapatsa chidwi ambiri mwa iwo kuti nawonso achitepo kanthu.
3Koma ndikutumiza abalewo kuti kukunyadirani kwathu pa zimenezi kutsimikizike kuti si kwachabe ndi kuti mukhale okonzeka monga ndinanenera.
4Pakuti nditabwera kumeneko ndi abale ena a ku Makedoniya, ndikukupezani kuti simunakonzeke, tingadzachite manyazi chifukwa chokudalirani. Koma amene angadzachite manyazi kwambiri ndi inuyo.
5Choncho ndinaganiza kuti nʼkofunika kupempha abale kuti adzakuchezereni ineyo ndisanafike, ndikuti adzatsirize kukonzekera mphatso zomwe munalonjeza kupereka mowolowamanja. Motero mphatsoyo idzakhala yokonzeratu, ndipo idzakhala mphatso yoperekedwa mowolowamanja, osati mokakamizidwa.
6Takumbukirani mawu awa: Amene adzala pangʼono, adzakololanso pangʼono, ndipo amene adzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.
7Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.
8Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino.
9Paja analemba kuti, “Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya.”
10Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu.
11Adzakulemeretsani pa zonse kuti mukhale owolowamanja pa nthawi zonse. Ndipo kuwolowamanja kwanu kudzera mwa ife, kudzakhala kuthokoza kwa Mulungu.
12Ntchito imene mukugwirayi siyongothandiza kokha anthu a Mulungu kupeza zosowa, komanso ikuthandiza kuti anthu ambiri ayamike Mulungu.
13Chifukwa cha ntchito imene mwawatsimikizira nokha, anthu ena onse adzayamika Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu kumene kumaonekera pamene mukuvomereza Uthenga Wabwino wa Khristu, ndiponso chifukwa chowagawira mowolowamanja iwowo pamodzi ndi wina aliyense.
14Ndipo iwowo adzakupemphererani mwachikondi chifukwa cha chisomo choposa chimene Ambuye wakupatsani.
15Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso zake zosaneneka!
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.