Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

2 MBIRI 11

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Rehobowamu atafika ku Yerusalemu anasonkhanitsa asilikali 180,000 a fuko la Yuda ndi Benjamini kuti akachite nkhondo ndi Israeli, kuti abwezeretse ufumu kwa Rehobowamu.
2Koma Yehova anayankhula ndi munthu wa Mulungu Semaya kuti,
3“Kawuze Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda ndi Aisraeli onse ali mu Yuda ndi Benjamini kuti,
4‘Yehova akuti: Musapite kukamenyana ndi abale anu. Pitani kwanu, aliyense wa inu, pakuti izi ndikuchita ndine.’ ” Choncho anamvera mawu a Yehova ndi kubwerera osapita kukamenyana ndi Yeroboamu.
5Rehobowamu amakhala mu Yerusalemu ndipo anamanga mizinda ya chitetezo iyi mu Yuda:
6Betelehemu, Etamu, Tekowa,
7Beti Zuri, Soko, Adulamu,
8Gati, Maresa, Zifi,
9Adoraimu, Lakisi, Azeka,
10Zora, Ayaloni ndi Hebroni. Iyi ndiye inali mizinda yotetezedwa ya Yuda ndi Benjamini.
11Iye anakhwimitsa chitetezo cha mizindayi ndipo anayikamo atsogoleri a ankhondo, pamodzi ndi chakudya, mafuta a olivi ndi vinyo.
12Mʼmizinda yonse anayikamo zishango zikuluzikulu ndi mikondo, ndipo anachititsa kuti mizindayo ikhale yamphamvu. Choncho iye amalamulira Yuda ndi Benjamini.
13Ansembe ndi Alevi a mʼmadera onse a Israeli anakhala mbali ya Rehobowamu.
14Alevi anasiya malo awo owetera ziweto ndi katundu wawo, ndi kubwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu chifukwa Yeroboamu ndi ana ake anawakana kukhala ansembe a Yehova.
15Ndipo iye anasankha ansembe akeake a pa malo opatulika ndi a mafano a mbuzi ndi mwana wangʼombe amene anapanga.
16Anthu ochokera fuko lililonse la Israeli amene anatsimikiza mitima yawo kufunafuna Yehova Mulungu wa Israeli, ankapitabe ku Yerusalemu kukapereka nsembe kwa Yehova, Mulungu wa makolo awo.
17Iwo analimbikitsa ufumu wa Yuda, ndipo anathandiza Rehobowamu mwana wa Solomoni kwa zaka zitatu. Pa nthawi imeneyi iye amatsatira zochita za Davide ndi Solomoni.
18Rehobowamu anakwatira Mahalati, amene abambo ake anali Yerimoti, mwana wa Davide, ndipo amayi ake anali Abihaili, mwana wa Eliabu, mwana wa Yese.
19Mkaziyo anamubereka ana aamuna awa: Yeusi, Semariya ndi Zahamu.
20Kenaka anakwatira Maaka, mwana wamkazi wa Abisalomu, amene anamubereka Abiya, Atai, Ziza ndi Selomiti.
21Rehobowamu ankamukonda Maaka mwana wa Abisalomu kuposa aliyense mwa akazi ake ndi azikazi. Iye anali ndi akazi 18, azikazi 60, ana aamuna 28 ndi ana aakazi 60.
22Rehobowamu anasankha Abiya mwana wa Maaka kuti akhale mtsogoleri pa abale ake, ndi cholinga choti adzakhale mfumu.
23Iye anachita mwanzeru, pomwaza ena mwa ana ake ku madera onse a Yuda ndi Benjamini, ndi ku mizinda yonse yotetezedwa. Iye anawapatsa zinthu zambiri ndiponso anawafunira akazi ambiri.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.