Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible

1 TIMOTEYO 4

Read Scripture freely. Divine Threads study for this chapter is coming later.

1Mzimu akunena momveka bwino kuti mʼmasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo ndi kutsatira mizimu yonyenga ndi zinthu zophunzitsidwa ndi ziwanda.
2Ziphunzitso zimenezi zimachokera ku chinyengo cha anthu onama, amene chikumbumtima chawo chinamatidwa ndi chitsulo cha moto.
3Iwo amaletsa anthu ukwati ndi kuwalamula kuti asamadye zakudya zina, zimene Mulungu analenga kuti amene anakhulupirira ndi kudziwa choonadi, azidye moyamika.
4Pakuti chilichonse chimene Mulungu analenga ndi chabwino, ndipo chilichonse chisasalidwe, akamachilandira moyamika,
5pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero.
6Ngati abale uwalangiza zimenezi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa mʼchoonadi cha chikhulupiriro ndi mʼchiphunzitso chabwino chimene wakhala ukutsata.
7Koma upewe nkhani zachabe ndi nthano za amayi okalamba; mʼmalo mwake udziphunzitse kukhala moyo wolemekeza Mulungu.
8Pakuti kulimbitsa thupi kumapindulitsapo pangʼono, koma moyo woopa Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo umene ukubwerawo.
9Amenewa ndi mawu odalirika ndi oyenera kuwalandira kwathunthu.
10Nʼchifukwa chake timagwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa, chifukwa tayika chiyembekezo chathu mwa Mulungu wamoyo, amene ndi Mpulumutsi wa anthu onse, koma makamaka wa amene amakhulupirira.
11Lamulira ndi kuphunzitsa zinthu zimenezi.
12Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
13Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa.
14Usanyozere mphatso yako yomwe inapatsidwa kwa iwe kudzera mʼmawu auneneri pamene gulu la akulu ampingo linakusanjika manja.
15Uzichita zimenezi mosamalitsa ndi modzipereka kwathunthu, kuti aliyense aone kuti ukupita mʼtsogolo.
16Samala kwambiri moyo wako ndi ziphunzitso zako. Uzichitabe zimenezi chifukwa ukatero, udzadzipulumutsa ndiponso udzapulumutsa okumvetsera.
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero — Open Chichewa Contemporary Bible. © 2002, 2016 Biblica, Inc.. Original source Bible: eBible.org/nya. Original translation by Biblica, Inc., freely available from Biblica and Open.Bible. The Scripture is licensed under Creative Commons Attribution–ShareAlike 4.0. Complete original publisher copyright notice. Scripture text adaptations remain under CC BY-SA 4.0. Biblica endorsement is not implied. The original publisher USFM formatting has been adapted to searchable verse rows. Section headings, footnote display markup and some paragraph styling are omitted; Scripture wording and the source-native verse numbers are preserved. Divine Threads research and Kids Corner content are separately authored, not yet translated in this language.